Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 4:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la cihema cokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lace pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

5. Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwerenao ku cihema cokomanako;

6. ndipo wansembeyo abviike cala cace m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova cakuno ca nsaru yocinga, ya malo opatulika.

7. Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la cofukiza ca pfungo lokoma, lokhala m'cihema cokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.

8. Ndipo acotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yaucimo, acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

9. ndi imso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso,

10. umo azikacotsera pa ng'ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe yopsereza.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 4