Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 4:17-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. nabviike cala cace m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, cakuno ca nsaru yocinga.

18. Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'cihema cokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.

19. Ndipo acotse mafuta ace onse, nawatenthe pa guwa la nsembe.

20. Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anacitira ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo wansembe awacitire cowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21. Ndipo aturutse ng'ombeyo kunja kwa cigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yaucimo ya kwa msonkhano.

22. Akacimwa mkuru, osati dala, pa cina ca zinthu ziti zonse aziletsa Yehova Mulungu wace, naparamula;

23. akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace, ndico tonde wopanda cirema;

24. naike dzanja lace pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.

25. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo ndi cala cace, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wace patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.

26. Ndipo atenthe mafuta ace onse pa guwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 4