Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 3:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo ana a Aroni azitenthe pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, iri pa nkhuni zimene ziri pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

6. Ndipo copereka cace cikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema;

7. akabwera nayo nkhosa kuti ikhale copereka cace, abwere nayo pamaso pa Yehova;

8. naike dzanja lace pamutu pa copereka cace, naiphe patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

9. Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ace, mcira wamafuta wonse, ataucotsa kufupi ku pfupa lao msana; naicotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

10. ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.

11. Ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe; ndico cakudya ca nsembe yamoto ya kwa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 3