Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 3:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo aike dzanja lace pa mutu wa copereka cace, ndi kuipha pa cipata ca cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

3. Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

4. ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.

5. Ndipo ana a Aroni azitenthe pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, iri pa nkhuni zimene ziri pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

6. Ndipo copereka cace cikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema;

7. akabwera nayo nkhosa kuti ikhale copereka cace, abwere nayo pamaso pa Yehova;

8. naike dzanja lace pamutu pa copereka cace, naiphe patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

9. Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ace, mcira wamafuta wonse, ataucotsa kufupi ku pfupa lao msana; naicotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

10. ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 3