Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 27:24-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Caka coliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lace lace.

25. Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika; sekeli ndi magera makumi awiri.

26. Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

27. Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wace; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.

28. Koma asacigulitse kapena kuciombola cinthu coperekedwa ciperekere kwa Mulungu, cimene munthu acipereka ciperekere kwa: Yehova, cotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wace wace; ciri conse coperekedwa ciperekere kwa Mulungu neopatulikitsa.

29. Asamuombole munthu woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.

30. Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zace za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 27