Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 27:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. koma poturuka m'caka coliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; ukhale wace wace wa wansembe.

22. Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wace wace;

23. pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wace wa kuyesa kwako kufikira caka coliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, cikhale cinthu copatulikira Yehova,

24. Caka coliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lace lace.

25. Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika; sekeli ndi magera makumi awiri.

26. Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

27. Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wace; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 27