Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 27:19-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo wakupacula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wace.

20. Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;

21. koma poturuka m'caka coliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; ukhale wace wace wa wansembe.

22. Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wace wace;

23. pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wace wa kuyesa kwako kufikira caka coliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, cikhale cinthu copatulikira Yehova,

24. Caka coliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lace lace.

25. Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika; sekeli ndi magera makumi awiri.

26. Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

27. Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wace; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.

28. Koma asacigulitse kapena kuciombola cinthu coperekedwa ciperekere kwa Mulungu, cimene munthu acipereka ciperekere kwa: Yehova, cotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wace wace; ciri conse coperekedwa ciperekere kwa Mulungu neopatulikitsa.

29. Asamuombole munthu woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.

30. Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zace za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.

31. Koma munthu akaombolatu kanthu ka limodzi la magawo khumiwo aonjezeko limodzi la magawo asanu.

32. Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, ziri zonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhale lopatulikira Yehova.

33. Asafunse ngati yabwino kapena yoipa, kapena kuisintha; koma akaisinthatu, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika zonse ziwiri; asamaiombola.

34. Awa ndi malamulo, amene Yehova anauza Mose, awauze ana a Israyeli, m'phiri la Sinai.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 27