Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 27:17-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Akapatula munda wace kuyambira caka coliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.

18. Akaupatula munda wace citapita caka coliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira caka coliza lipenga, nazicepsako pa kuyesa kwako.

19. Ndipo wakupacula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wace.

20. Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;

21. koma poturuka m'caka coliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa ciperekere kwa Mulungu; ukhale wace wace wa wansembe.

22. Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wace wace;

23. pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wace wa kuyesa kwako kufikira caka coliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, cikhale cinthu copatulikira Yehova,

24. Caka coliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lace lace.

25. Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika; sekeli ndi magera makumi awiri.

26. Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 27