Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 26:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. ndipo mudzacita nayo mphamvu yanu cabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatse zace, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zace.

21. Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zocimwa zanu.

22. Popeza ndidzatumiza cirombo ca kuthengo pakati pa inu, ndipo cidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nicidzacepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.

23. Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;

24. Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zoipa zanu.

25. Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakucita cilango ca cipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.

26. Pamene ndityola mcirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mcembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.

27. Ndipo mukapanda kundimvera Ine, cingakhale ici, ndi kuyenda motsutsana nane;

28. Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.

29. Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.

30. Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31. Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za pfungo lanu lokoma.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 26