Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 25:8-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.

9. Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la citetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.

10. Ndipo mucipatule caka ca makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muciyese caka coliza lipenga; ndipo mubwerere munthu ali yense ku zace zace, ndipo mubwerere yense ku banja lace.

11. Muciyese caka ca makomi asanuco coliza lipenga, musamabzala, kapena kuceka zophuka zokha m'mwemo; kapenakuceka mphesa zace za mipesa yosadzombola.

12. Popeza ndico caka coliza lipenga; muciyese copatulika, mudye zipatso zace kunja kwa munda.

13. Caka coliza lipenga ici mubwerere nonse ku zace zace.

14. Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana;

15. monga mwa kuwerenga kwace kwa zaka, citapita coliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.

16. Monga mwa kucuruka kwa zaka zace uonjeze mtengo wace, ndi monga mwa kucepa kwa zaka zace ucepse mtengo wace; pakuti akugulitsa powerenga masiku ace.

17. Musamasautsana, koma uope Mulungu wako; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

18. M'mwemo mucite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita; ndipo mudzakhala m'dzikomo okhazikika.

19. Dziko lidzaperekanso zipatso zace, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi k'ukhalamo okhazikika.

20. Ndipo mukadzati, Tidzadyanji caka cacisanu ndi ciwiri? taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;

21. pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu caka cacisanu ndi cimodzi, ndipo cidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.

22. Ndipo mubzale caka cacisanu ndi citatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira caka cacisanu ndi cinai, mpaka zitacha zipatso zace mudzadya zasundwe.

23. Ndipo asaligulitse dziko cigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.

24. Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 25