43. Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.
44. Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo amuna ndi akazi.
45. Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anu anu.
46. Ndipo muwayese colowa ca ana anu akudza m'mbuyo, akhale ao ao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israyeli, musamalamulirana mozunza.
47. Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera cuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa pfuko la banja la mlendo;
48. atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ace amuombole;
49. kapena mbale wa atate wace, kapena mwana wa mbale wa atate wace amuombole, kapena mbale wace ali yense wa banja lace amuombole; kapena akalemera cuma yekha adziombole yekha.
50. Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira caka adadzigulitsa kwa iye kufikira caka coliza lipenga; ndipo mtengo wace ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.
51. Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndarama zakumuombola zocokera ku ndalama zomgulazo.
52. Ndipo zikamtsalira zaka pang'ono kufikira caka coliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zace abwezere mtengo wace wakumuombola.
53. Akhale naye monga wolipidwa caka ndi caka; asamamlamulira momzunza pamaso pako,
54. Ndipo akapanda kumuombola motero, azituruka caka coliza lipenga, iye ndi ana ace omwe.
55. Pakuti ana a Israyeli ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.