30. Ndi munthu ali yense wakugwira nchito iri yonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wace.
31. Musamagwira nchito iri yonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zoo nse.
32. Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzicepetse; tsiku lacisanu ndi cinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.
33. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
34. Nena ndi ana a Israyeli, kuti, Tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi uno wacisanu ndi ciwiri pali madyerero a misasa a Yehova, masiku asanu ndi awiri.
35. Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira nchito ya masiku ena.
36. Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lacisanu ndi citatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira nchito ya masiku ena.