Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 22:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. ndi ali yense wokhudza cinthu cokwawa cakudetsedwa naco, kapenanso munthu amene akamdetsa naco, codetsa cace ciri conse;

6. munthu wokhudza ciri conse cotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lace ndi madzi.

7. Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pace adyeko zoyerazo, popeza ndizo cakudya cace.

8. Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.

9. Potero asunge cilangizo canga, angasenzepo ucimo, ndi kufera m'mwemo, pakuciipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo,

10. Mlendo asadyeko copatulikaco; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa nchito, asadyeko copatulikaco.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 22