Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 21:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu cifukwa ca wakufa mwa anthu a mtundu wace;

2. koma cifukwa ca abale ace eni eni ndiwo, mai wace, ndi atate wace, ndi mwana wace wamwamuna, ndi mwana wace wamkazi, ndi mbale wace;

3. ndi cifukwa ca mlongo wace weni weni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse cifukwa ca iwowa.

4. Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wace, asadzidetse, ndi kudziipsa,

5. Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kucecerera ndebvu zao, kapena kudziceka matupi ao.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 21