Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 2:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Monga copereka ca zipatso zoyamba muzipereka izi: koma asazifukize pa guwa la nsembe zicite pfungo lokoma.

13. Ndipo copereka cako ciri conse ca nsembe yaufa uzicikoleretsa ndi mcere; usasowe mcere wa cipangano ca Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mcere.

14. Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kuca, zoumika pamoto, zokonola.

15. Ndipo uthirepo mafuta, ndi kuikapo libona; ndiyo nsembe yaufa.

16. Ndipo wansembe atenthe cikumbutso cace, atatapa pa tirigu wace wokonola, ndi pa mafuta ace, ndi kutenga libano lace lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 2