34. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
35. Musamacita cisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wace, kulemera kwace, kapena kucuruka kwace.
36. Mukhale naco coyesera coona, miyeso yoona, era woona, bini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto.
37. Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwacita; Ine ndine Yehova.