Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 18:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Usamabvula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.

9. Usamabvula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.

10. Usamabvula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.

11. Usamabvula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.

12. Usamabvula mlongo wa atate wako; ndiye wa cibale ca atate wako.

13. Usamabvula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako.

14. Usamabvula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wace; ndiye mai wako.

15. Usamabvula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamambvula.

16. Usamabvula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako.

17. Usamabvula mkazi ndi mwana wamkazi wace; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wace, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wace kumbvula; ndiwo abale; cocititsa manyazi ici.

18. Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wace, kumbvuta, kumbvula pamodzi ndi mnzace, akah ndi moyo mnzaceyo.

19. Usamasendera kwa mkazi kumbvula pokhala ali padera cifukwa ca kudetsedwa kwace.

20. Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

21. Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto cifukwa ca Moleke, usamaipsa dzina la Mulungu wako: Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 18