Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 18:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Usamabvula mkazi ndi mwana wamkazi wace; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wace, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wace kumbvula; ndiwo abale; cocititsa manyazi ici.

18. Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wace, kumbvuta, kumbvula pamodzi ndi mnzace, akah ndi moyo mnzaceyo.

19. Usamasendera kwa mkazi kumbvula pokhala ali padera cifukwa ca kudetsedwa kwace.

20. Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

21. Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto cifukwa ca Moleke, usamaipsa dzina la Mulungu wako: Ine ndine Yehova.

22. Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; conyansa ici.

23. Ndipo usamagonana ndi nyama iri yonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; cisokonezo coopsa ici.

24. Musamadzidetsa naco cimodzi ca izi; pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;

25. dziko lomwe lidetsedwa; cifukwa cace ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo.

26. Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osacita cimodzi conse ca zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu;

27. (pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazicita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa)

Werengani mutu wathunthu Levitiko 18