Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. ndipo wansembe aturuke kumka kunja kwa cigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda Yakhate yapola pa wakhateyo;

4. pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi, ubweya wofiira, ndi hisope;

5. ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;

6. natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;

7. nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lace, namuche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.

8. Ndipo iye wakutiayeretsedwe atsuke zobvala zace, namete tsitsi lace lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kucigono, koma agone pa bwalo la hema wace masiku asanu ndi awiri.

9. Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lace lonse la pamutu pace, ndi ndebvu zace, ndi nsidze zace, inde amete tsitsi lace lonse; natsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nakhale woyera.

10. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge ana a nkhosa awiri, amuna opanda cirema, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamkazi wa caka cimodzi wopanda cirema, ndi atatu a magawo khumi a ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa mafuta.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14