Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 13:42-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lace la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lirikubuka pakati pa dazi lace la pamutu, kapena la pamphumi.

43. Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati cotupa cace ca nthenda ciri cotuuluka pa dazi la pa mutu wace, kapena la pamphumi pace, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;

44. ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amuchetu wodetsedwa; nthenda yace iri pamutu pace.

45. Ndipo azing'amba zobvala zace za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pace lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wace wa m'mwamba, napfuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!

46. Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pace pakhale kunja kwa cigono.

47. Ndiponso ngati nthenda yakhate iri pa cobvala caubweya, kapena cathonje;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 13