15. Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namuche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate.
16. Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,
17. ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amuche woyera wanthendayo; ndiye woyera.
18. Ndipo pamene thupi liri ndi cironda pakhungu pace, ndipo capola,
19. ndipo padali cironda pali cotupa coyera, kapena cikanga cotuuluka, pamenepo acionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone,
20. ndipo taonani, ngati cioneka cakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lace lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'cirondamo.