Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 13:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2. Ngati munthu ali naco cotupa, kapena nkhanambo, kapena cikanga pa khungu la thupi lace, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lace, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ace ansembe;

3. ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lace, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namuche wodetsedwa.

4. Koma ngati cikanga cikhala cotuwa pa khungu la thupi lace, ndipo cikaoneka cosapitirira khungu, ndi tsitsi lace losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;

5. ndipo wansembe amuonenso tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;

6. ndipo wansembe amuonenso tsikulacisanu ndi ciwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amuche iye woyera, ndiyo nkhanambo cabe; ndipo atsuke zobvala zace, ndiye woyera;

7. koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsakwa wansembe kuti achedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;

8. ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amuche wodetsedwa, ndilo khate.

9. Pamene nthenda yakhate iri mwa munthu, azimfikitsa kwa wansembe;

10. ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali cotupa coyera pakhungu, ndipo casanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pacotupa pali mnofu wofiira,

11. ndilo khate lakale pa khungu la thupi lace, ndipo wansembe amuche wodetsedwa; asambindikiritse popeza ali wodetsedwa.

12. Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wace kufikira mapazi ace, monga momwe apenyera wansembe;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 13