Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 11:24-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo izi zikudetsani: ali yense akhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;

25. ndipo ali yense akanyamulako nyama ya mtembo wace azitsuka zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

26. Nyama iri yonse yakugawanika ciboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; ali yense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.

27. Ndipo iri yonse iyenda yopanda ciboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; ali yense wokhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

28. Ndipo iye amene akanyamula mtembo wace atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.

29. Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wace;

30. ndi gondwa, ndi mng'anzi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi mfuko.

31. Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; ali yense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

32. Ndipo ciri conse cakufa ca izi cikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale cipangizo camtengo, kapena cobvala, kapena cikopa kapena thumba, cipangizo ciri conse cimene agwira naco nchito, acibviike m'madzi, ndipo cidzakhala codetsedwa kufikira madzulo; pamenepo cidzakhala coyera.

33. Ndipo ciri conse ca izi cikagwa m'cotengera ciri conse cadothi, cinthu cokhala m'mwemo cidetsedwa, ndi cotengeraco muciswe.

34. Cakudya ciri conse cokhala m'mwemo, cokonzeka ndi madzi, cidzakhala codetsedwa; ndi cakumwa ciri conse m'cotengera cotere cidzakhala codetsedwa.

35. Ndipo kanthu ka mtembo wace kakagwa pa zinthu ziri zonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mcembo kapena mphika wobvundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.

36. Koma kasupe kapena citsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa.

37. Ndipo kanthu ka mtembo wace kakagwa pa mbeu yofesa, ikati ifesedwe, idzakhala yoyera.

38. Koma akathira madzi pa mbeuyi, ndi kanthu ka mtembo wace kakagwapo, muiyese yodetsedwa.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 11