Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 8:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Lipenga kukamwa kwako, Akudza ngati ciombankhanga, kulim bana ndi nyumba ya Yehova; cifukwa analakwira cipangano canga, napikisana naco cilamulo canga.

2. Adzapfuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisrayeli tikudziwani.

3. Israyeli wacitaya cokoma, mdani adzamlondola.

4. Analonga mafumu, koma sikunacokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golidi wao, kuti akalikhidwe.

5. Mwana wa ng'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?

6. Pakuti ici comwe cafumira kwa Israyeli; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwana wa ng'ombe wa Samariya adzaphwanyika-phwanyika.

7. Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kabvumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzaturutsa ufa; cinkana iuturutsa, alendo adzaumeza.

8. Israyeli wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati cotengera coti munthu sakondwera naco.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 8