1. Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.
2. Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lacitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pace.
3. Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kuturuka kwace kwakonzekeratu ngati matanda kuca; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.