Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 5:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Imvani ici, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israyeli; cherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti ciweruzoci cinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabora.

2. Ndipo opandukawo analowadi m'zobvunda; koma Ine ndine wakuwadzudzula onsewo.

3. Ndimdziwa Efraimu, ndi Israyeli sandibisikira; pakuti Efraimu iwe, wacita citole tsopano, Israyeli wadetsedwa.

4. Macitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wacitole uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova.

5. Ndipo kudzikuza kwa Israyeli kudzamcitira umboni pamaso pace; cifukwa cace Israyeli ndi Efraimu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao.

6. Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikuru kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwacokera.

7. Anacita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana acilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.

8. Ombani mphalasa m'Gibeya, ndi lipenga m'Rama; pfuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.

9. Efraimu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mapfuko a Israyeli ndadziwitsa codzacitikadi.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 5