Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 4:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Anthu anga afunsira ku mtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wacigololo wawalakwitsa, ndipo acita cigololo kucokera Mulungu wao.

13. Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi miniali, ndi mkundi; popeza mthunzi wace ndi wabwino, cifukwa cace ana anu akazi acita citole, ndi apongozi anu acita cigololo.

14. Sindidzalanga ana anu akazi pocita citole iwo, kapena apongozi anu pocita cigololo iwo; pakuti iwo okha apambukira padera ndi akazi acitole, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa kucitole; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa camutu.

15. Cinkana iwe, Israyeli, ucita citole, koma asaparamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.

16. Pakuti Israyeli wacita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwana wa nkhosa ku thengo lalikuru.

17. Efraimu waphatikana ndi mafano, mlekeni.

18. Cakumwa cao casasa, acita citole kosalekeza; akuru ao akonda manyazi kwambiri.

19. Mphepo yamkulunga m'mapiko ace, ndipo adzacita manyazi cifukwa ca nsembe zao.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 4