Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 2:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wocitidwa-cifundo.

2. Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindiri mwamuna wace; ndipo acotse zadama zace pankhope pace, ndi zigololo zace pakati pa maere ace;

3. ndingambvule wamarisece, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati cipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;

4. ndipo ana ace sindidzawacitira cifundo; pakuti iwo ndiwo ana acigololo.

5. Pakuti mai wao anacita cigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anacita camanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine cakudya canga, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi cakumwa canga.

6. Cifukwa cace taonani, ndidzacinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ace.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 2