Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 2:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wocitidwa-cifundo.

2. Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindiri mwamuna wace; ndipo acotse zadama zace pankhope pace, ndi zigololo zace pakati pa maere ace;

3. ndingambvule wamarisece, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati cipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;

4. ndipo ana ace sindidzawacitira cifundo; pakuti iwo ndiwo ana acigololo.

5. Pakuti mai wao anacita cigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anacita camanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine cakudya canga, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi cakumwa canga.

6. Cifukwa cace taonani, ndidzacinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ace.

7. Ndipo adzatsata omkonda koma osawakumika, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.

8. Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumcurukitsira siliva ndi golidi, zimene anapanga nazo Baala.

9. Cifukwa cace ndidzabwera ndi kucotsa tirigu wanga m'nyengo yace, ndi vinyo wanga m'nthawi yace yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langi, zimene zikadapfunda umarisece wace.

10. Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ace pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 2