Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 14:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Israyeli, bwerera kumka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.

2. Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Cotsani mphulupulu zonse, nimulandire cokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati: ng'ombe.

3. Asuri sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitil dzanenanso kwa nchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza cifundo.

4. Ndidzaciritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamcokera.

5. Ndidzakhala kwa Israyeli ngati mame; adzacita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yace ngati Lebano.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 14