Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 13:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere m'dziko la Aigupto, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.

5. Ndinakudziwa m'cipululu, m'dziko lotentha kwambiri.

6. Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; cifukwa cace anandiiwala Ine.

7. Cifukwa cace ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira.

8. Ndidzakomana nao ngati cimbalangondo cocilanda ana ace, ndi kung'amba cokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; cirombo cidzawamwetula.

9. Israyeli, cikuononga ndi ici, cakuti utsutsana ndi Ine, cithandizo cako.

10. Iri kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?

11. Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamcotsanso m'ukali wanga.

12. Mphulupulu ya Efraimu yamangika, cimo lace lisungika.

13. Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asacedwe mobalira ana.

14. Ndidzawaombola ku, mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako iri kuti? manda, cionongeko cako ciri kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 13