Cinkana abala mwa abale ace, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kucokera kucipululu; ndi gwero lace lidzaphwa, ndi kasupe wace adzauma, adzafunkha cuma ca akatundu onse ofunika.