Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 13:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo tsopano aonjeza kucimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo nchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone ana a ng'ombe.

3. Cifukwa cace adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi woturuka kukafwambira.

4. Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere m'dziko la Aigupto, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.

5. Ndinakudziwa m'cipululu, m'dziko lotentha kwambiri.

6. Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; cifukwa cace anandiiwala Ine.

7. Cifukwa cace ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira.

8. Ndidzakomana nao ngati cimbalangondo cocilanda ana ace, ndi kung'amba cokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; cirombo cidzawamwetula.

9. Israyeli, cikuononga ndi ici, cakuti utsutsana ndi Ine, cithandizo cako.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 13