Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 13:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Bfraimu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza m'Israyeli; koma pamene anaparamula mwa Baala, anafa.

2. Ndipo tsopano aonjeza kucimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo nchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone ana a ng'ombe.

3. Cifukwa cace adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi woturuka kukafwambira.

4. Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere m'dziko la Aigupto, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.

5. Ndinakudziwa m'cipululu, m'dziko lotentha kwambiri.

6. Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; cifukwa cace anandiiwala Ine.

7. Cifukwa cace ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira.

8. Ndidzakomana nao ngati cimbalangondo cocilanda ana ace, ndi kung'amba cokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; cirombo cidzawamwetula.

9. Israyeli, cikuononga ndi ici, cakuti utsutsana ndi Ine, cithandizo cako.

10. Iri kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?

11. Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamcotsanso m'ukali wanga.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 13