Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 12:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zace, adzambwezera monga mwa macitidwe ace.

3. M'mimba anagwira ku citende ca mkuru wace, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;

4. inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Beteli, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;

5. ndiye Yehova Mulungu wa makamu, cikumbukilo cace ndi Yehova.

6. M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga cifundo ndi ciweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 12