Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 12:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Efraimu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse acurukitsa mabodza ndi cipasuko, ndipo acita pangano ndi Asuri, natenga mafuta kumka nao ku Aigupto,

2. Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zace, adzambwezera monga mwa macitidwe ace.

3. M'mimba anagwira ku citende ca mkuru wace, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;

4. inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Beteli, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;

5. ndiye Yehova Mulungu wa makamu, cikumbukilo cace ndi Yehova.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 12