4. Anena mau akulumbira monama, pakucita mapangano momwemo; ciweruzo ciphuka ngati zitsamba zowawa m'micera ya munda.
5. Okhala m'Samariya adzaopera cifanizo ca ana a ng'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ace adzamva naco cisoni, ndi ansembe ace amene anakondwera naco, cifukwa ca ulemerero wace, popeza unacicokera.
6. Adzacitengeranso ku Asuri cikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efraimu adzatenga manyazi, ndi Israyeli adzacita manyazi ndi uphungu wace.
7. Ndipo Samariya, mfumu yace yamwelera ngati thobvu pamadzi.
8. Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo cimo la Israyeli, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.
9. Israyeli, wacimwa kuyambira masiku a Gibeya; pomwepo anaimabe; nkhondo ya pa ana a cosalungama siinawapeza ku Gibeya.