17. Pakuti ciwawa cidacitikira Lebano cidzakukuta, ndi cionongeko ca nyama cidzakuopsa; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitidwira dziko, mudzi, ndi onseokhalamo.
18. Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, ata panga matafano osanena mau?
19. Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka Kodi ici ciphunzitsa? Taona cakutidwa ndi golidi ndi siliva, ndi m'kati mwace mulibe mpweya konse.
20. Koma Yehova ali m'Kacisi wace wopatulika; dziko lonse lapansi ale, cete pamaso pace.