Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 2:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Tsoka wakuninkha mnzace cakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!

16. Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; cikho ca dzanja lamanja la Yehova cidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako,

17. Pakuti ciwawa cidacitikira Lebano cidzakukuta, ndi cionongeko ca nyama cidzakuopsa; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitidwira dziko, mudzi, ndi onseokhalamo.

18. Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, ata panga matafano osanena mau?

Werengani mutu wathunthu Habakuku 2