Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 1:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti taonani, ndiukitsa Akasidi, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira, pa citando ca dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwao mwao.

7. Ali oopsa, acititsa mantha, ciweruzo cao ndi ukulu wao zituruka kwa iwo eni.

8. Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati ciombankhanga cofulumira kudya.

9. Adzera ciwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mcenga,

10. Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga liri lonse; popeza aunjika dothi, nalilanda.

11. Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, oadzalakwa ndi kuparamula, iye amene aiyesa mphamvu yace mulungu wace.

12. Si ndinu wacikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.

13. Inu wa maso osalakwa, osapenya coipa, osakhoza kupenyerera cobvuta, mupenyereranji iwo akucita mocenjerera, ndi kukhala cete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;

Werengani mutu wathunthu Habakuku 1