Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 1:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga liri lonse; popeza aunjika dothi, nalilanda.

11. Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, oadzalakwa ndi kuparamula, iye amene aiyesa mphamvu yace mulungu wace.

12. Si ndinu wacikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.

13. Inu wa maso osalakwa, osapenya coipa, osakhoza kupenyerera cobvuta, mupenyereranji iwo akucita mocenjerera, ndi kukhala cete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini;

14. ndi kuyesa anthu ngati nsomba za m'nyanja, ngati zokwawa zopanda wakuzilamulira.

15. Aziwedza zonse ndi mbedza, azigwira m'ukonde wace, nazisonkhanitsa m'khoka mwace; cifukwa cace asekera nakondwerera.

16. Cifukwa cace aphera nsembe ukonde wace, nafukizira khoka lace, pakuti mwa izi gawo lace lilemera, ndi cakudya cace cicuruka.

17. Kodi m'mwemo adzakhuthula m'ukonde mwace osaleka kuphabe amitundu?

Werengani mutu wathunthu Habakuku 1