Ndipo panali caka ca mazana asanu ndi limodzi kudza cimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anacotsa cindwi lace pacingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi.