Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 6:19-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiri ziwiri za mtundu wao ulowetse m'cingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.

20. Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiri ziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.

21. Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, oudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo.

22. Cotero anacita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anacita.

Werengani mutu wathunthu Genesis 6