Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 6:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali pamene anthu anayamba kucuruka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo,

2. kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.

3. Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.

4. Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

5. Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukuru pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

6. Ndipo Yehova anamva cisoni cifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anabvutika m'mtima mwace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 6