Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 6:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali pamene anthu anayamba kucuruka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo,

2. kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.

3. Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.

4. Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

5. Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukuru pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

6. Ndipo Yehova anamva cisoni cifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anabvutika m'mtima mwace.

7. Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva cisoni cifukwa ndapanga izo.

8. Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.

9. Mibadwoya Nowandiiyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yace; Nowa anayendabe ndi Mulungu.

10. Ndipo Nowa anabala ana amuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.

11. Ndipo dziko lapansi linabvunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi ciwawa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 6