Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 50:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. cifukwa kuti ana ace amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pace, kwa Efroni Mhiti, patsogolo pa Mamre.

14. Ndipo ataika atate wace, Yosefe mabwera ku Aigupto, iye ndi abale ace, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wace.

15. Ndipo pamene abale ace a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamcitira iye.

16. Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti,

17. Muziti cotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kucimwa kwao, cifukwa kuti anakucitirani inu coipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa aka polo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.

18. Ndiponso abale ace anamuka namgwadira pamaso pace; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.

19. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndiri ine kodi m'malo a Mulungu?

Werengani mutu wathunthu Genesis 50