Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 49:30-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. m'phanga liri m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamre, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efroni Mhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pace:

31. pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wace; pamenepo anaika Isake ndi Rebeka mkazi wace: pamenepo ndinaika Leya:

32. munda ndi phanga liri m'menemo, zinagulidwa kwa ana a Heti.

33. Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ace amuna, anafunya mapazi ace pakama, natsirizika, nasonkhanizidwa kwa anthu a mtundu wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 49