Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 49:24-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Koma uta wace unakhala wamphamvu,Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwaNdi manja a Wamphamvu wa Yakobo.(Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)

25. Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iweNdi madalitso a Kumwamba,Madalitso a madzi akuya akukhala pansi,Madalitso a mabere, ndi a mimba.

26. Madalitso a atate wakoApambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,Kufikira ku malekezero a patari a mapiri a cikhalire;Adzakhala pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ace.

27. Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;M'mamawa adzadya comotola,Madzulo adzagawa zofunkha.

28. Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israyeli: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wace anawadalitsa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 49