Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 49:14-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Isakara ndiye buru wolimba,Alinkugona pakati pa makola;

15. Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,Ndi dziko kuti linali lokondweretsa;Ndipo anaweramitsa phewa lace kuti anyamule,Nakhala kapolo wakugwira nchito ya msonkho,

16. Dani adzaweruza anthu ace,Monga limodzi la mafuko a Israyeli.

17. Dani adzakhala njoka m'khwalala,Songo panjira,Imene iluma zitende za kavalo,Kuti womkwera wace agwe cambuyo.

18. Ndadikira cipulumutso canu, Yehova.

19. Ndi Gadi, acifwamba adzampsinja iye;Koma iye adzapsinja pa citende cao.

20. Ndi Aseri, cakudya cace ndico mafuta,Ndipo adzapereka zolongosoka zacifumu.

21. Nafitali ndi nswala yomasuka;Apatsa mau abwino.

22. Yosefe ndi nthambi yobala,Nthambi yobala pambali pa kasupe;Nthambi zace ziyangayanga palinga.

23. Eni uta anabvutitsa iye kwambiri,Namponyera iye, namzunza:

24. Koma uta wace unakhala wamphamvu,Ndi mikono ya manja ace inalimbitsidwaNdi manja a Wamphamvu wa Yakobo.(Kucokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israyeli,)

25. Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iweNdi madalitso a Kumwamba,Madalitso a madzi akuya akukhala pansi,Madalitso a mabere, ndi a mimba.

26. Madalitso a atate wakoApambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,Kufikira ku malekezero a patari a mapiri a cikhalire;Adzakhala pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ace.

27. Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;M'mamawa adzadya comotola,Madzulo adzagawa zofunkha.

28. Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israyeli: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wace anawadalitsa.

29. Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga liri m'munda wa Efroni Mhiti,

30. m'phanga liri m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamre, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efroni Mhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pace:

31. pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wace; pamenepo anaika Isake ndi Rebeka mkazi wace: pamenepo ndinaika Leya:

Werengani mutu wathunthu Genesis 49