Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 49:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Adamanga mwana wa kavalo wace pampesa,Ndi mwana wa buru wace pa mpesa wosankhika;Natsuka malaya ace m'vinyo,Ndi copfunda cace m'mwazi wa mphesa.

12. Maso ace adzafiira ndi vinyo,Ndipo mana ace adzayera ndi mkaka.

13. Zebuloni adzakhala m'doko la kunyanja;Ndipo iye adzakhala doko la ngalawa;Ndipo malire ace adakhala pa Zidoni.

14. Isakara ndiye buru wolimba,Alinkugona pakati pa makola;

15. Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,Ndi dziko kuti linali lokondweretsa;Ndipo anaweramitsa phewa lace kuti anyamule,Nakhala kapolo wakugwira nchito ya msonkho,

16. Dani adzaweruza anthu ace,Monga limodzi la mafuko a Israyeli.

17. Dani adzakhala njoka m'khwalala,Songo panjira,Imene iluma zitende za kavalo,Kuti womkwera wace agwe cambuyo.

18. Ndadikira cipulumutso canu, Yehova.

Werengani mutu wathunthu Genesis 49